Banja lapha mwana pofuna kulemera

Advertisement
Lilongwe

Apolisi ku Nanthenje munzinda wa Lilongwe amanga banja lina kamba kopha mwana wawo wamamuna wa zaka ziwiri ngati chizimba chomwe sing’anga wina unawauza kuti apange ndicholinga choti alemera.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi munzinda wa Lilongwe, Hastings Chigalu, awiriwa omwe onse ndi a zaka 25, azindikilidwa ngati a Ivy Elinati komaso amuna awo Mphatso Malinde omwe ndi bambo omupeza mwana ophedwayu.

A Chigalu ati awiriwa adapita kwa sing’anga wina m’dziko la Mozambique ndicholinga chofuna kulemera komwe adauzidwa kuti akuyenera aphe mwana wawo ndikupitsa mtembo wake. Potsatira chizimbachi awiriwa adanyamula mwana wawo kupita naye kwa sing’angayo ndipo mkati mwa ulendo adamupha pomupotokora khosi.  

Chatsitsa dzaye nchakuti awiriwa atapha mwanayo, anayimbira thenifolo sing’angayo kumudziwitsa kuti achita monga momwe adawauzira ndipo ali m’njira kuwapititsira mtembo, koma sing’angayo adawakanira ponena kuti sadakwaniritse zizimba zina asanaphe mwanayo.

Apa banjali lidagwidwa njakata, ndipo lidapanga chiganizo chobwerera ku mudzi kwawo komwe lidakanama kuti mwanayo wafa yekha ali ku mbuyo kwa mayi ake, koma akuluakulu ena sadakhutitsidwe ndipo adakadziwitsa a polisi za nkhaniyi.

Apolisi atawapanikiza, awiriwa adawulura kuti adaphadi mwanayo, ndipo zotsatira za chipatala zidasonyeza kuti mwanayo anafa kaamba kobanika atapotokoledwa khosi.

Posachedwapa a Elinati omwe ndi ochokera m’mudzi wa Chimbwala m’boma la Mchinji komaso a Nalinde ochokera m’mudzi wa Chikuwa ku Lilongwe akawonekera ku khothi komwe akayankhe mlandu wakupha.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.