Makolo ena ku Thyolo ataya mwana chifukwa cha umphawi

Advertisement
Thyolo

Makolo ena ataya mwana wa mwezi umodzi pa chipatala chachikulu cha Thyolo, ponena kuti sakwanitsa kumusamala.

M’neneri wa apolisi m’bomali, Sergeant Rabecca Kashoti wati m’mawawu, munthu wina anapeza mwanayo akulira kwambiri pamalo oimitsira njinga zamoto kufupi ndi wodi ya ana.

A Kashoti ati atavundukula chofunda chake anapeza kalata yomwe makolowa anasiya.

“Pepani kwa aliyense amene angakwanise kumulera mwanayu. Ifeyo monga makolo ake sitikwanitsa kumusamala mwanayu kamba ka mabvuto a zachuma, chonde aliyense wakufuna kwabwino amusamale mwanayu ngati wake. Dzina lake ndi Glory koma mutafuna mutha kumusintha dzinalo,” izi ndi zina zomwe zili pa Kalatayi.

Makolowa anati sanafune kutaya mimba koma chomwe chavuta kwambiri ndi chithandizo, ndipo anthu akufuna kwabwino amusamale mwanayo.

Mneneri wa a Police a Kashoti ati alumikizana kale ndi ofesi yoona za chisamaliro cha anthu m’bomali kuti apeze njira yomusamalira mwanayu.

Mneneri wa ofesi ya zaumoyo m’bomali a Fanuel Makina watsimikiza za nkhaniyi, ndipo wati ofesi yawo ichita chothekela kuwonetsetsa kuti mwanayi wapeza chithandizo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.