Apezeka olakwa, chigamuro pa 3 September

Advertisement
Mzimba

Anthu awiri omwe bwalo la milandu ku Mzimba lidawapeza olakwa pa mlandu wakuba moopseza akuyembekezeka kudzalandira chigamulo mwezi wa mawa pa 3 September 2024.

Devie Harry adapezeka olakwa pamilandu yonse inayi pomwe Lukas Golosi adapezeka wolakwa pamilandu itatu, boma litapempha bwalo kuti lichotse a Golosi pamlandu wachinayi, ponena kuti padalakwika kuti dzina lake lipezeke pa zikalata za mulandu wa chinai. 

Oyimira boma pa milandu, Aubrey Maganga, adauza bwaloli kuti awiriwa, pamodzi ndi anzawo omwe sakupezeka pakati pa mwezi wa June ndi July chaka chino, akhala akuba ndi kuchita umbanda m’malo osiyana siyana m’bomali.

Bwaloli lidamvanso kuti awiriwa, pa 2 June, 2024 adakathyola nyumba ya namwino wina komwe adamuvulaza ndikumubera ma laputopu awiri, table imodzi, matayala awiri anjinga ya moto ndi ndalama zokwana K160,000. 

Mbali ya boma inatinso pa June 16, awiriwa adaberanso munthu wina wabizinesi ndalama zokwana K5 Miliyoni ndi mafoni awiri a m’manja. 

Pomwe pa mlandu wachitatu, omangidwawa pa 4 July adabera wabizinesi wodziwika bwino, Bonface Zimba, ndalama zokwana K21.2 miliyoni ndi mafoni atatu ndikuwavulaza kwambiri mmutu ndi manja.

Pamulandu wa chinai awiriwa pa Julayi 19 adaba mafoni amabatani okwana 195, mafoni asanu amakono ndi K4 miliyoni kwa ochitanso bizinesi wina.

Maganga adati odandaula anayiwo adagonekedwa ku chipatala cha m’boma la Mzimba komwe malandira chithandizo, pomwe Bonface adawatumiza ku chipatala chachikulu cha Mzuzu komwe adakhala masiku atatu ali chikomokere. 

Awiriwa atapezeka kuti ndi wolakwa, woweruza mulandu first grade Radson Gamariel analengeza kuti azapereka chigamulo chake pa September 3, 2024. Komabe Malawi24 yapeza kuti awiri akayankhanso mlandu wofuna khupha munthu (Attempt to mudder) kubwalo lalikulu.

Golosi wazaka 31, amachokera mmudzi wa Chathina, Mfumu yayikulu Nsamala, M’boma la Balaka pomwe Harry akuchokera mmudzi mwa Fikani Mfumu yayikulu Mabuka , M’boma la Mulanje.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.