MCP yamana utsogoleri kwa ofuna kupanga nawo mgwirizano

Advertisement
Chimwendo Banda

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chatsindika kuti icho chili ndi chikoka chodzapambana moposela ma voti 70 pa 100 aliwonse ndipo maso sakuyang’ana mgwirizano koma kwa ofuna kutero asaganize zodzatsogolera popeza a Lazarus Chakwera okha ndi amene ali oyenera.

Polankhula pa msonkhano wa ndale lachitatu ku Nchalo m’boma la Chikwawa, mlembi wamkulu wa chipanichi a Richard Chimwendo Banda ati khomo kwa ofuna mgwirizano ndi lotsekula koma osati kutsogolera mgwirizano.

A Chimwendo anawonjezera kuti omwe ukuoneka kuti utha kukhala mgwirizano pakati pa zipani za DPP, UTM, AFORD, UDF ndi chilinganizo chopanda tsogolo chifukwa alibe akadaulo aluso.

M’mau ake, oyankhulira chipanichi a Jessie Kabwira ati chipani chawo chidzapambana kuposa theka la mavoti onse, ulamulirooo wa a Chakwera ukangothana ndi mavuto amene ali pano.

A Kabwila ati a chipani cha DPP akunamiza anthu kuti adzapambana mu masankho a 2025 pamene akukanika kuyendetsa chipani chawo chomwe anthu anasiya kuchikonda ponena kuti umboni wawoneka ku msonkhano wawukulu omwe wachitika sabata yatha.

Iwo anati chipani cha DPP chakanika kutsogoza achinyamata kupeleka mpata kwa amayi, komanso mipando yambiri anthu alowa mosapikisana kusocheza kutha kwa chikoka cha chipanichi.

“Umeneuja si msonkhano wawukulu okasankha atsogoleri umeneuja ndi msonkhano okatsimikizira atsogoleri, kunali ku Confirmation osati convention” anatelo a Kabwila.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.