Anthu anayi amwalira pa ngozi ku Zomba

Advertisement
Malawi24

Anthu anayi amwalira ndipo khumi awagonenka pachipatala cha Zomba Central Hospital m’boma la Zomba, atavulala pa ngozi yomwe yachitika lero m’bomalo.

Malingana ndi aPolisi oyang’anira za pa nseu nchigawochi, a Augustine Chakanika ati ngoziyi yachitika pamene minibus yomwe anthuwa adakwera anagubuduzika kawiri pa 8 Miles m’bomali.

A Chakanika ati ngoziyi yachitika kamba koti oyendetsa Minibus yo, a Wilson Jemba amathamanga mopyola muyeso zomwe zidachititsa kuti minibus yo ichite ngozi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.