Takonzeka kuthambitsana ndi Bullets – Arrows

Advertisement
CAF Champions League

Timu ya Red Arrows ya m’dziko la Zambia yati ndiyokonzeka kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa masewero a mu CAF Champions League omwe achitike mawa (18 August 2024) pa bwalo la za masewero la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.

Mphunzitsi wa Red Arrows, Kalililo Kakonje wauza atolankhani kuti timuyake ndiyokonzeka kugonjetsa Nyasa Big Bullets mawa pano.

Kakonje wati timuyi yachita zonse zokonzekera ndipo ikuyembekezera masewerowa apamwamba. 

Koma polankhula pa mwambo wa atolankhani okonzekera masewerawa, Kakonje wati Arrows sitengera momwe adani awo adachitira mmbuyomu koma kuyang’ana kwambiri masewerowa.

Padakali pano wotsogolera wosewera (Captain) wa Arrows, Saddam Phiri wati pakalipano wosewera onse ali ndi moralo yayikulu ndipo akonzeka kuthana ndi timu ya Bullets.

M’mau ake wachiwiri kwa mphunzitsi wa Nyasa Big Bullets, Heston Munthari wanenetsa kuti iwo pokhala akatswili a ligi yaku Malawi akonzeka ndipo safuna kalikonse koma chipambano.

“Ngakhale nthawi yomwe timasewera mu quarter finals ya FDH Bank Cup, aliyense amati sitichita bwino koma tidakwanitsa kupambana 1-0, ngakhaleso mawa tili ndi chikhulupiriro kuti tizapambana,” watero Munthali. 

Timu ya Red Arrows yakhala ikuchita bwino pamasewero osiyanasiyana mdziko lawo pomwe anakwanitsa kugonjetsa timu ya Kabwe Warriors 4-1 kuti itenge chikho cha Black Charity Shield.

Timu ya Bullets yakhala isakuchita bwino mu masewero asanu ndi anayi omaliza muligi ya TNM ndipo ili pa nambala 5 mu ligiyi ndi ma pointi okwana 24.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.