Nyekhwe! Dzina labambo anga ayi – Paul Gadama waletsedwa

Advertisement

Pomwe kwangotsala maola ochepa kuti konveshoni ya chipani cha Democratic Progressive (DPP) iyambe, a Paul Gadama agwidwa njakata pomwe mwana wa malemu Aaron Gadama watenga chiletso chowaletsa kugwiritsa ntchito dzina la bambo awoli ponena kuti sanali bambo awo.

Malingana ndi zikalata za ku khothi zomwe tsamba lino lawona, Joseph Gadama pamodzi ndi akubanja akufuna a Paul adzigwiritsa ntchito dzina lina ponena kuti malemu Gadama sanali bambo awo.

Kudzera mwa loya wawo, Silvester Ayuba James, banja la a Gadama lawuza khothi kuti m’mbuyomu lakhala likuwuza a Paul kuti akayezetse kuti atsimikizedi ngati malemuwo analidi bambo awo koma ati mkuluyu wakhala akukana.

Banjali lati choncho nkofunika kuti a Paul adzigwiritsa ntchito dzina la Nsikula omwe akuti ndiye bambo awo osati Gadama.

A Paul akupikisana nawo pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP m’chigawo chapakati ku msonkhano wa ukulu wa chipanichi omwe ukuyamba Lamulungu lino munzinda wa Blantyre.

Malemu Aaron Gadama anali m’modzi mwa akuluakulu a chipani cha MCP ndipo anafa mchaka cha 1983 pangozi ya galimoto m’boma la Mwanza ngakhale kuti anthu ena amakhulupilira kuti anachita kuphedwa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.