Mbava zitatu zoopsa kwambiri zamangidwa ku Mzimba

Advertisement
Malawi24

Apolisi ku Mzimba akusunga m’chitokosi amuna atatu powaganizila kuti akhala akuchita zamtopola m’bomali pobera komanso kuvulaza anthu ochita ma bizinesi m’miyezi ya June ndi July chaka chino.

Atatuwa ndi a Luka Golosi a zaka 31, Davie Harry a zaka 49, komanso Patrick Moma a zaka 41. 

Malinga ndi m’neneri wa polisi ya Mzimba Peter Botha, M’miyezi ya June ndi July, 2024, atatuwa komanso anzawo ena omwe kusakidwabe, akhala akuba ndalama, ma foni ndi TV m’nyumba mwa anthu ena abizinesi komanso kuvulaza anthuwa.

Botha wati apolisi adagwira atatuwa malo osiyanasiyana atachita kafukufuku wakuya ndipo apezanso zina mwazinthu zomwe zidabedwa. 

Golosi anagwidwa pa 24 July,2024 ndipo kwao ndi ku Balaka pamene Moma anamangwidwa pa 26 July,2024 pa Mzimba boma ndipo Harry anagwidwa pa 31July,2024 ndipo kwawo nku Mulanje.

Anthuwa awatsekulira mulandu wa Kuba moopseza.

Wochita malonda wodziwika bwino Bonface Zimba anakhapidwa kwambiri ndi anthu akuba moopsezawa ndipo panopa akadali mu uluru osaneneka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.