Mtsikana wa zaka 17 apha mwana pofuna kukwanilitsa chizimba

Advertisement
Malawi24

Malodza! Mtsikana wa zaka 17 ali m’manja mwa apolisi ku Lilongwe pomuganizira kuti wapha mwana wa zaka 10 pofuna kukwanilitsa chizimba chomwe anauzidwa ndi chibwenzi chake pa masamba anchezo.

Wofalitsa nkhani pa polisi ya Lingadzi a Cassim Manda, ati mtsikanayu anali paubwezi ndi munthu wina yemwe mpaka pano sanadziwike. Ubwenzi wa awiriwa unali wa pa masamba anchezo kamba koti chiyambira sanakumanepo.

Mamunayo wakhala akulamula mtsikanayu kuchita zinthu zodabwitsa kwambiri kuphatikizapo kumuuza kuti agone ndi mwamuna kanayi nakatelo amutumizire umuna wa mamuna ogona nayeyo, zomwe mtsikanayu wakhala akupanga mosanyinyilika.

Chatsitsa dzaye nchakuti posachedwapa mamunayo anauza mtsikanayu kuti mizimu ikufuna nsembe ya mwana ndipo ngati sapanga zimenezo, iye pamodzi ndi abale ake awona malodza osasimbika.

Powopa kuwona mazangazime, mtsikanayu adetenga mwana woyandikana naye nyumba ku Mtandire, kupita naye ku malo ena ogona alendo, komwe adamumangilira ndikumupha pomubaya katatu.

Wogwira ntchito pa malopo ndi yemwe adapeza thupi la mwanalo pansi pa bed ndipo kenaka adadziwitsa apolisi omwe amanga woganiziridwayo yemwe posachedwapa akawonekere ku bwalo la milandu kuti akayankhe mlandu wakupha.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.