Sindidamenye Pop Young – wakanitsitsa Phyzix

Advertisement
Noel Chikoleka

Woyimba Noel Chikoleka yemwe adayimba nyimbo ya “Makofi” ndipo amadziwika kwambiri ndi dzina loti Phyzix, watsutsa mphekesera zoti iye adamenya woyimba nzake Pop Young chifukwa chokakamiza nkazi yemwe adapita naye kokayimba kuti amulore chibwezi.

Potsatira mphekeserazi zomwe zakhala zikuveka m’masamba anchezo, Phyzix watulutsa chikalata chofotokoza momwe zinakhalira ku malo ochitira zisangalaro a Blues Elephant munzinda wa Blantyre Loweluka lapitali.

Woyimbayu wati patsikuli iye anafika ku maloku ndi anthu ena asanu kukayimba pa phwando la mayimbidwe lomwe linakozedwa ndi kampani yopititsa patsogolo mayimbidwe m’dziko muno ya Urban Music People (UMP).

Iye wati mayimbidwe ali nkati, woyimba Pop Young yemweso anaitanidwaso kuti akayimbe, adadyelera maso ndikufusira m’modzi mwa akazi omwe adabwera limodzi ndi “Man Phyzo” koma nyenyeziyo inakanitsitsa kugwa nchikondi ndi woyimba wakumpototu.

“Popizo” sanavetse kuti wakanidwa ndipo anakakamirabe mpaka nkaziyo atawona kuti zafika posawuzana adakanena za nkhaniyi kwa Phyzix yemwe sanachedwe koma kukamufikira.

Ngakhale zili choncho, Phyzix wakanitsitsa kuti adamenya Pop Young ponena kuti, “Chofunika kwambiri, panalibe chiwawa kapena kumenyana panthawi yonseyi. Anthu ambiri adawona zomwe woyimbayu (Pop Young) adachita ndipo zidajambulidwa pa kanema wa CCTV, ndipo zilipo.

“Phyzix adamaliza nkhaniyi mwamtendere, ndikutsimikizira (Pop Young) kuti alibe maganizo oyipa pa iye ndipo adamukumbutsa (Pop Young) kuti m’mbuyomu wakhala akumuthandizira pa mayimbidwe ake kudzera m’masamba ake anchezo.”

Pomaliza Phyzix kudzera m’kalatayi wachenjeza oyimba omwe angoyamba kumene kuti apewe kudzimva kuti ali ndi ufulu ochita chili chonse chomwe angafune, ponena kuti akuyenera kumalemekeza malire awo makamaka kwa azimayi.

Phyzix asanatulutse kalatayi Pop Young anali atafotokoza kale zomwe zinachitika ponena kuti nkaziyu akunenedwayo ndi yemwe adamufikira iye ndipo anati iye sanamufusire nkaziyo, zomwe zikusemphana ndi zomwe wanena woyimba wa “Mwantinti.”

Pop Young adalemba pa tsamba lake la fesibuku kuti, “Mtsikana wina anandipeza ndikundipatsa ndipo ndinamuyankhura monga momwe ndimachitira ndi onditsata onse ndikapita ku show. Kenaka m’modzi mwa oyimba akulu akulu anabwera kudzandikwenya kufuna kundimenya kuti ndamuyankhula mkazi wake.”

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.