Ndiloleni ndiyimeso – Muluzi

Advertisement
UDF

2025 kuli gule! Zisankho zapatatu zitionetsa kathu! Yemwe anati mwana mbu, make mbu analinga atapsola diso ku chipani cha United Democratic Front (UDF). Inu, ali ndi mwana agwilitse.

Atupele Muluzi yemwe m’chaka cha 2022 adatula pansi udindo wake ngati mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF), wasonyeza chidwi chake chofunitsitsa kubweleraso pa udindowu.

Mlembi wamkulu wa chipani cha UDF Kandi Padambo watsimikizira nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti Muluzi wawonetsa chidwi chake pomwe watenga zikalata zomwe zikupelekedwa kwa anthu omwe akufuna kukapikisana nawo pa ma udindo osiyanasiyana ku nsonkhano waukulu wa chipanichi.

Malingana ndi Padambo, Atupele yemwe ndi mwana wa mtsogoleri wa kale wa dziko lino, Bakili Muluzi, ngati angapambane akhozaso kudzayimirira chipanichi pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chaka cha mawa.

Posachedwapa, a Muluzi analemba pa tsamba lawo la fesibuku kuti, “Ndinapanga chisankho chopuma kaye ngati mtsogoleri wa chipani cha UDF ndi cholinga chakuti ndipereke mwayi kwa aliyense ofuna kutenga maudindo otsogolera chipanichi kuti tonse tikapikisane mofanana ku convention yomwe ikubwera mwezi wa August chaka chino.”

Potsatira kulengezaku, katswiri pankhani za ndale George Phiri wachenjeza a Muluzi kuti ngati angasankhidwe pa udindo wa mtsogoleri wa chipani cha UDF, ayembekezere mikwingwilima pa ntchito yokopaso chikhulupiriro cha anthu komanso kutsitsimutsa chipani cha UDF.

Pakadali pano, wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa zokozekera msonkhano waukulu wa UDF, a Aisha Adams, ati zonse zili nchimake kuti chipanichi chichititse nsonkhanowu pa 3 August 2024.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.