Matako, anthu enanso awiri agonabe m’chitokosi cha Police

Advertisement
Lilian Matako, Zuberi Chitete and Ishmael Chitete

Bwalo la Senior Resident Magistrate Joshua Nkhono ku Balaka lakana kupeleka belo kwa mayi Lilian Matako, a Zuberi Chitete komanso a Ishmael Chitete.

Anthuwa akuwaganizira kuti adachita zinthu zofuna kuvulaza munthu.

Powonekera ku bwalo la milandu lero masana, anthuwa akana kuvomera mulandu umene bwalo la milandu likuwazenga.

Anthuwa adanjatidwa zitadziwika kuti adathandizana kupeleka chilango chomumangilira mumtengo komanso kumuthira madzi a Chitedze mwana wa zaka 9 chifukwa chokuba ndalama yokwana K2,000.

A Matako, omwe ndi a zaka 28 ndipo ndi mayi ake a mwanayu amachita bizinesi ndipo akuti adasiya ndalamayo kuchipinda kwawo. Koma pobwelera, mayiyu sadaipeze ndalama ija ndipo izi zidapangitsa kuti amupanikize ndi mafunso mwanayo kufikira pomwe adaulura kuti adatengadi ndalamayo.

Izi akuti zidadzetsa mkwiyo mwa mayiyu ndipo adagwilizana ndi anyamatawa kuti amulange mwanayu pomumangilira mumtengo kenako kumuthira madzi a Chitedze.

Mulanduwu ubweleranso m’mbwalo la milandu lachisanu likubwelari pomwe bwalori lidzawunikile pa pempho lawo la belo.

Oganizilidwawa amachokera m’mudzi mwa Kanyumbaka, mfumu yaikulu Sawali m’boma lomweri la Balaka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.