Gibo Pearson wapulumuka pangozi ya galimoto

Advertisement

Oyimba Gibo Pearson wapulumuka pa ngozi ya pansewu pomwe galimoto yomwe amayendetsa inasadabuzika Lolemba ku Blantyre.

Woyimbayu amachoka kokaimba ku Zomba. Malingana ndi uthenga omwe tawona ochokera kwa woyimbayu yemwe amadziwika ndi nyimbo za lokolo, ngoziyi yachitika pa malo ena otchedwa Mapanga mu nsewu wa Blantyre-Zomba.

Woyimba wa ku Phalombe-yu wati atafika pa malowa paulendo wake opita kokaimbaso ku Bangwe munzinda wa Blantyre, ma buleki komaso chiwongolero cha galimoto yomwe amayendetsa zonse zidasiya kugwira ntchito pakamodzi.

“Lero ndikuchoka koimba ku Zomba pamene ndimapitanso kubangwe kukaimba nawo pa Bangwe Festival ndikudusa pamabanga pafupi ndi FASA galimoto yanga ma break komanso chiongolero zinasiya kugwila ntchito zomwe zinachitisa kuti ndilephere kuchita control galimoto mpaka galimoto ndikutembenuzika.mwayi palibe wavulala pangozoyi,” watelo Pearson.

Pakadali pano, anthu ochuluka makamaka m’masamba anchezo akumufunira zabwino woyimbayu yemwe posachedwapa wathyakula nyimbo ya “Galu Ndine” yomwe ikuvinidwa m’malo osiyanasiyana.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.