Zikhulupiriro zikubwezeretsa m’buyo ntchito yolimbana ndi nthenda ya Khate – Thindwa

Advertisement
leprosy

Ogwira ntchito pa Chipatala chachikulu cha Rumphi ati ntchito yothana ndi nthenda ya Khate ikuyenda pang’onopang’ono m’bomali chifukwa cha zikhulupiriro zomwe anthu alinazo zomwe zikulepheretsa a chipatala  kufikira anthu ochuluka.

Poyankhurana ndi nyumba yolemba nkhani ino, owona za matenda apa khungu a Elizabeth Anderson Thindwa anati anthu okhala m’bomali amakhulupirira kuti Khate ndi nthenda ya kale ya m’baibulo ndipo yemwe ali ndi nthendayi akuyenera kukhala kutali ndi anthu oyandikananawo kuti asawapatsire.

A Nthindwa anawonjezera ponena kuti ena akapezeka ndi nthendayi amapita kaye kwa a sing’anga adzitsamba kukaombedza m’malo mothamangira ku chipatala kuti akapeze thandizo loyenera.

“Pakadali pano, chiwerengero cha anthu odwala Khate kuno ku Rumphi n’chotsika chifukwa choti anthu alibe uthenga okwanira okhudzana ndi nthendayi.Tikamayenda m’midzimu zimakhala zovuta kugwira ntchito yathu moyenera chifukwa anthu ambiri sakudziwa za nthendayi chifukwa ali ndi maganizo oti odwala Khate ndi munthu otembeleledwa,” iwo anatero.

Iwo anati ngakhale zinthu zili chomwechi, akuyesetsa kufalitsa uthenga okhudzana ndi nthendayi ponseponse kuti anthuwa akhale ndi uthenga oyenera, monga pokhala ndi maphunziro pa wailesi yowulutsa mawu ya Rumphi n’cholinga chophunzitsa anthu zokhudzana ndi nthendayi.

Iwo anati anthu omwe anapezeka ndi nthendayi amadandaura kutalika kwa mtunda oyenda popita kuchipatala komano vutoli linatha popeza anthuwa anayamba kulandira ndalama yoti adziyendera ndi thandizo kuchokera ku World Bank.

A Thindwa adapempha boma komanso mabungwe kuti awathandizire kuphunzitsa anthu onse a za umoyo ogwira ntchito m’bomali kuti akhale ndi uthenga oyenera potengera kuti ambiri sakudziwabe za Khate zomwe zikupangitsa kuti nthendayi idzipezeka mochedwa mwa anthu.

Chiwerengero cha anthu odwala Khate pa Chipatala cha Rumphi ndi chotsika, omwe akudwala nthendayi alipo atatu. Anthu onse analipo asanu ndipo awiri anachira atamwa mankhwala mwandondomeko yoyenera.

Khate ndi nthenda yomwe imagwira munthu aliyense.

Zizindikiro zake ndi kutuluka ziwawu zosapweteka pa thupi, dzanzi komanso kutuluka zilonda zapakhungu zolimba. Munthu odwala nthendayi ayenera kupewa kumwa mowa, kusuta ndipo amayenera kudya zakudya za magulu onse atatu.