Reggae sasungunula ngati Sobo – Jah Rhyno

Advertisement
Hope Chiusiwa

Oyimba komanso kukanyanga nsambo mu chamba cha Reggea Jah Rhyno yemwe dzina lake lenileni ndi Hope Chiusiwa wa mugulu la Tuff Lions wati ayitanidwa kachiwiri ku kayimba ku Tanzania ku Zanzibar Festival mu August, chifukwa Reggae yawo sasungunula ngati sobo.

Malingana ndi Rhyno, sichilichonse chomwe chimamveka ndi zin’gwenyen’gwenye zonga reggae nde kuti ndi reggae. 

“Anthu ambiri amasiyanitsa reggea music ya ku Malawi makamaka yochokera ku Balaka, Chileka ndimadera ena. Komanso sinkhani yakochokera koma kudziwa chimene ukuyimba,” watero Jah Rhyno yemwe amakhala ku Lilongwe. 

Hope Chiusiwa
Jah Rhyno: Reggae yathu sitisungunula ngati sobo.

Anapitilira kufotokoza kuti, “pali anthu ena amangoyimba reggae chifukwa ena angowauza kuti iyi ndi reggae koma kuwafunsa kuti chambachi chinachokera kuti ndipo anayambitsa ndani sangayankhe.” 

Kutsatira ukadaulo omwe gulu la Tuff Lions band lidaonetsa ku Tanzania ku Zanzibar Festival mu 2022 motsogozedwa ndi Blasto chawakomeranso okonza mwambowu kuyitana gululi kachikena. 

Ngati Njira imodzi yosaka thandizo la ndalama kuti akapezeke ku mwambowo  gululi lakonza phwando lamayimbidwe lomwe likukutchedwa ‘Road to Zanzibar Festival’ pa 28 July, 2024 ku Glalle Gardens ku Lilongwe. 

Malingana ndi Chester Maganizo yemwe amathandiza gululi  wati ku phwandoku kukhala oyimba monga Nepman, Blasto, Nepman, Macelba, JayJay Cee, Chizmo ndi ena ambiri. 

“Anthu azabwere mwaunyinji chifukwa oyimba onsewa palibe azagwiritse ntchito CD onse azabakilidwa ndi band yathu pogwiritsa ntchito zida,”anatero Maganizo. 

Tuff Lions ndi gulu lokhalo m’dziko muno lomwe lagwira ntchito ndi oyimba ambiri akunja maka ochokera ku Jamaica ngati Turbelence, Luciano ndi Everton Blender, kungotchula ochepa chabe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.