Matako komanso anyamata awiri akawonekera ku bwalo la milandu Lachiwiri

Advertisement
Lilian Matako, Ishmael Chitete, Zuberi Chitete

Mayi Lilian Matako, a Ishmael Chitete komanso a Zuberi Chitete akawonekera ku bwalo la milandu Lachiwiri likubwelari komwe akayankhe mulandu opanga zinthu zofuna kuvulaza munthu.

Malingana ndi mneneri wa apolisi ku Balaka, Inspector Gladson M’bumpha, anthu atatuwa ali mmanja mwa apolisi powaganizira kuti anathandizana kupeleka chilango chomumangilira mumtengo komanso kumuthira madzi a Chiteze mwana wamkazi wa zaka 9 chifukwa chokuba ndalama yokwana K2000.

A Matako, a zaka 28 omwenso ndi mayi wa mwanayu ndi ochita malonda ndipo akuti adasiya ndalama kuchipinda kwawo.Koma atabwelera pakhomo, mayiyu sadaipeze ndalama ija ndipo izi zidapangitsa kuti amupanikize mwana wawoyo ndi mafunso kufikira pamene adavomera kuti adabadi ndalamayo.

Chifukwa chodzadzidwa ndi mkwiyo, mayiyu mothandizana ndi a Zuberi Chitete a zaka 18 komanso a Ishmael Chitete a zaka 20 adamangilira mwanayu mumtengo asadamuthile madzi a Chitedze.

Oganizilidwawa amachokera m’mudzi mwa Kanyumbaka, mfumu yaikulu Sawali m’boma lomweri la Balaka.

Advertisement

One Comment

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.