Matako, anthu ena awiri amangidwa pa mlandu wozunza mwana wa zaka 9

Advertisement
Malawi24

Wolankhulira Polisi ya Balaka, Gladson M’pumpha watsimikizira nyumba zowulutsa mawu m’dziko muno kuti anthu enanso awiri amangidwa m’mamawa wa Lamulungu kutsatira nkhani yokhudzana ndi mayi Matako omwe anawanjata dzulo chifukwa chozunza mwana wawo wamkazi atampeza kuti anawabera ndalama yokwana K2,000 

Anthu omwe anjatidwawa omwe ndipachibale ndi a Ishmael Chitete a zaka 20 ndi Zuberi Chitete azaka 18, ndipo amachokera mmudzi mwa Kunyumbayaka mfumu yayikulu Sawali m’boma la Balaka.

Awiriwa ndiwomwe akuwaganizira kuti anathandizira kugwira ndikumangilira mwanayu manja ndi miyendo kumtengo pomwe amamupanga zankhazazi pomuthira madzi osakaniza ndi chitedze.

Anthu atatuwa akuyembekezeka kukayankha mlandu wopanga zinthu zofuna kuvulaza munthu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.