Ng’ombe ya eid yakankhira mnyamata ku ndende 

Advertisement
Malawi24

Mnyamata wa zaka 23, Chikondi Maluwa amugamula kuti akagwire jere kwa zaka zitatu, bwalo la milandu la Midima ku Limbe mu mzinda wa Blantyre litamupeza olakwa pa mulandu okuba Ng’ombe ya Eid.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za polisi ya Limbe, a Aubrey Singanyama ati ogamulidwayu anaba Ng’ombeyo yomwe inali ya Eid ku Mpingwe mu mzinda wa Blantyre.

Bwalo la milandu la Midima linapeza a Maluwa olakwa ndipo awagamula kukakhala ku ndende zaka zitatu pofuna kupeleka phunziro kwa ena ngakhale ogamulidwayu anapempha kuti alandile chilango chochepa chifukwa sanavute kuvomera mulandu wake.

A Maluwa amachokera mmudzi mwa a Tsoka, kwa mfumu yayikulu (T/A) Thomas M’boma la Thyolo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.