Abida Mia akapikisana nawo pampando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha MCP

Advertisement
Abida Mia

Phungu wa ku nyumba ya malamulo m’dera la Chikwawa Nkombezi, Abida Mia, abwera poyera kuti akapikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) pansonkhano waukulu wachipani omwe uchitike mwezi wa mawa wa August.

Polankhula ndi Malawi24 a Mia omwenso ndi nduna ya za madzi ndi ukhondo ati ndizoona kuti akapikisana nawo pampando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha MCP.

Iwo ati achita izi potsatira kuti anthu ambiri m’dziko muno akhala akuwapempha kuti akapikisane nawo pachisankho chosankha adindo atsopano achipani cha MCP.

“Ndafuna kuti nditsimikize kwa anthu amene amandikonda kuti komanso kwa anthu omwe akhala akundipempha kuti ndikapikisane nawo pachisankho pansonkhano waukulu wachipani cha MCP kuti tsopano ndamvomera kuti ndikapikisana nawo pampando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani,” datero a Mia.

Chipani cha MCP chichititsa msonkhano wake waukulu kuyambira pa 8 mpaka pa 10 August chaka chino kumene akasankhe atsogoleri omwe azitsogolera chipanichi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.