Ophunzira wafa atagundidwa ndi njinga yamoto

Advertisement
Malawi24

Ophunzira wina wa zaka khumi (10) m’boma la Phalombe, wafa atagundidwa ndi njinga yamoto dzulo Lamulungu pomwe oyendetsa njingayi anakanika kuyiwongolera kamba kothamanga kwambiri.

M’neneri wa polisi ya Phalombe, a Jimmy Kapanja, watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti ophunzirayu yemwe dzina lake Chrispin Makalani, yemwe anali kuphunzira pa sukulu ya pulayimale ya Namikango.

Malingana ndi m’neneliyu, ophunzirayu anagundidwa pa malo ochitira malonda a Nalingula pomwe woyendetsa njingayu, yemwe dzina lake ndi McDonald Banda, anakanika kuyiwongolera bwino pomwe amafuna kukhota kamba kothamanga kwambiri.

Kapanja wati ophunzirayu adavulala kwambili mmutu ndipo anamwalira atangofika naye kuchipata chachikulu cha m’bomalo.

Kuphatikiza apo Kapanja anati wanjinga yamotoyu anagundanso munthu wina yemwe dzina lake ndi Damison Chimtengo, yemwe anavulala kwambiri pa fupa lolumikiza pa bondo ndi phazi.

Pakadali pano, Chimtengo akulandira thandizo la mankhwala ku chipatala.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.