Apolisi amanga nyamata wama iPhone

Advertisement
TikTok Daddy

Mnyamata amene amadziwika bwino ndi dzina loti iPhone Daddy patsamba la mchezo la TikTok, Innocent Sengimana wazaka 23, wamangidwa ndi apolisi ku Area 3 munzinda wa Lilongwe kamba kobera anthu ndalama zokwana 5 miliyoni kwacha powanamiza kuti awapatsa lamya za mtundu wa iPhone 13.

Mneneli wa apolisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu atsimikiza zankhaniyi ndipo iye watinso mkuluyu amalephera kubweza ndalama zolipilira magalimoto omwe iye wakhala akubwereka kuti azijambulira 

zinthu zake zomwe amayika pa masamba a mchezo.

Malingana ndi a Chigalu, m’nyamatayu wakhala akutolera ndalama kudzera pa tsamba lake lamchezo lomwe limadziwika ndi dzina loti “innocentjumajayi” ndipo iye adatenganso lamya ziwiri za mtundu wa iPhone zomwe amati awagulitsire koma sadaonekenso.

Mnyamatayu atamva kuti apolisi akumusakasaka pa zimenezi iye amathawathawa.

Chigalu anati tsiku lomwe nyamatayu amamangidwa anachita kumupulumutsidwa pomwe anthu amafuna amuphe panthawi yomwe iye amkathamangitsana ndi apolisi.

Pompano nyamatayu akaonekera ku bwalo la milandu komwe iye akayankhe pa mulandu wakuba.

Wolemba: Ben Bongololo 

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.