Neba za ligi sakupanga nawo: Bullets 0 KB 0

Advertisement
TNM Super League

Maule, yang’anani kumbali. Chaka chino timu yanu za ligi sikupanga nawo. Kapena mwina tingoti kwa iwo sinayambe. Khalani kumadikila raundi yachiwiri, paja timu yanu ndi kumadzulo. Chifukwa zimene zawachitikiranso lero ku Lilongwe, mavuto aja akupitilirabe. 

Pamene chaka chatha anali a katswiri mpaka kukolola zikho zinayi, chaka chino zikuoneka kuti sizili bwino ku ma pale. Timu ya Nyasa Big Bullets lero yakhumudwitsanso owatsatira italepherana ndi timu ya Kamuzu Barracks. 

Pa masewero amene anachitikira pa bwalo la Civo mu mzinda wa Lilongwe, timu ya Bullets inabwera mosaka chipambano kamba ka zokhoma zimene anaziona sabata latha pomwe analepherana ndi timu ya Creck mu mzinda omwewu wa Lilongwe. Zotsatira zimene sizinawapatse owakonda chilimbikitso poona ndi pendapenda amene akhala akumuona mu ligi. 

Ngakhale izi zinali chomwechi, sikuti timu ya Bullets inabwera ndi moto weniweni. Anali anyamata a KB amene amaoneka ngati akufuna kulanga anyamata a Bullets. Koma podziwa chipongwe ndi chipolowe chimene angathe kuchiona akagonja, anyamata a Bullets anachilimika kuti asadzokedwe koyamba chigoli. 

Panali patatha mphindi khumi ndi zisanu (15) pamene anyamata a Bullets anakhala ngati akumbukira chomwe anadzera pa Civo. Apa ndi pamene anakhala ngati nawo ayamba kubwenza moto mpaka anapeza mwayi wa kona yachiwiri mu mphindiyi koma sunaphule kanthu. 

Matimuwa anatsatana ndithu, wina kupanikiza ndi winanso kubwenza mpaka mphindi 45 pamene oyimbira anaona kuti ndi chanzeru kuti tsopano anyamata akapumulire. Koma ngakhale zinali chonchi ndi kuti mpirawu uli ngati chabe ndeu ya zitsiru, panalibe anamuphophola mzake ngakhale amapeza mwayi. 

Mu chigawo chachiwiri, anyamata a Bullets ndiwo anakhala ngati amvera kukhazikidwa pansi ndi malango a Pasuwa. Patangotha mphindi zisanu chigawochi chitayamba, mnyamata Babatunde Adepoju adatsala pang’ono kumwetsa koma msungigolo wa KB Hastings Banda adayima mochirikiza kuonetsetsa kuti anyamatawa asamwetse. 

Njala ya chigoli imene anyamata a Bullets sikuti idaphula kanthu ngakhale iwo amaoneka ngati akudziwa chomwe akuchita mu chigawo chachiwiri. M’mene mphindi 90 zimakwana ndiye kuti okonda timuyi atayamba kale kufinya makolona kukonzekera tsiku lina la chitonzo pomwe ena adali kufuulira kwa Mulungu wawo kuti awadutsitse mu nyengo yokhoma ngati iyi. 

Oyimbira adaonjezera mphindi zingapo, koma zonse zinali chabe ndipo m’mene amauthetsa mpira ndiye kuti timu ya Bullets itapitiriza ndi rekodi yake yolepherana ndi ma timu ena mu ulendo uno okha wa ligi kufika pa masewero asanu ndi awiri (7).

Pamene a Bullets amachoka pa Civo mozyolika, timu ya FOMO ndikuti itakhoma Moyale ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi pa bwalo la Mulanje pomwe Baka City nayo yakhoma Bangwe ndi zigoli ziwiri kwa chilowere.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.