MCP ikulemekezabe masiku 21 okumbukira a Chilima, ngakhale yatuluka kukamba za Convention 

Advertisement
Moses Kunkuyu

Pamene dziko la Malawi lili m’masiku 21 okhudza imfa ya amene anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko, a Saulos Chilima, chipani cha MCP loweluka chinavumbuluka kufotokoza za msonkhano wawo waukulu ndipo ati akukonzekera mwa kachetechete ndicholinga chofuna kulemekeza masiku 21 amene mtsogoleri wa dziko yemwenso ndi mtsogoleri wa chipanichi a Lazarus Chakwera analamulira.

Mu msonkhano wa atolankhani lero m’modzi mwa akulu akulu ku chipanichi, a Moses Kunkuyu, yemwenso ndi nduna yofalitsa nkhani ati chipani cha MCP chatuluka kukamba za dongosolo la msonkhano wawo waukulu omwe uchitike pa 8 ndi pa 10 August 2024 ku Bingu International Convention Centre (BICC) mu mzinda wa Lilongwe, koma molemekeza masiku 21okhudza infa ya yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko.

A Kunkuyu anati zambiri sizinakambidwe pofuna kulemekeza masiku 21 okhudza imfayi.

Wapampando yemwe ayendetse dongosolo la msonkhano waukuluwu, a Kezzie Msukwa ati onse ofuna kukapikisana nawo pa mipando ayamba kukatenga zikalata za chidwi chawo chodzapikisana kuyambira pa 1 July ndi kukasiyidwa pasanafike pa 15 July 2024, ponena kuti ayeneranso kupeleka ndalama yofunsilira mpando omwe afuna kukapikisana nawo.

Malingana ndi a Msukwa, ofuna kuyimira mpando wa mtsogoleri wa chipani akuyenera kupeleka 5 miliyoni kwacha ndi achiwiri awo akuyenera kupeleka 2.5 miliyoni kwacha 

Mpando wa Mlembi wamkulu ndi msungi chuma akuyenela kupeleka 2 miliyoni kwacha, ndi achiwiri awo adzapeleka 1 miliyoni kwacha komanso ma Director adzapeleka 500 sauzande kwacha aliyense.

Iwo anaonjezera kuti onse amene ali ndi ulumali adzapeleka theka la ndalama yofunsilira mipando yomwe akuyenera kupeleka.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.