Fleetwood Haiya ndi masomphenya ake, FAM ikusintha

Advertisement
FAM

Bungwe loyendetsa mpira wa miyendo la Football Association of Malawi (FAM), motsogozedwa ndi mtsogoleri wake a Fleetwood Haiya, lavomeleza chigawo cha ku m’mawa kukhala imodzi mwa zigawo zake.

Izi zikutanthauza kuti zigawozi zawonjezereka kufika pa khumi (10) ndipo anthu omwe adzivotera mtsogoleri wa bungweli awonjezerekanso mwa zina. Ma boma a chigawo chatsopanochi akuphatikiza ma boma a Zomba, Machinga, Balaka, Mangochi ndi Phalombe

Kusinthaku kwavomelezedwa kudzela mu mkumano wawo wawukulu omwe wachitikira ku Mkopola Lodge m’boma la Mangochi komwe avomelezanso masomphenya a Bungweli.

Mtsogoleri wa bungwe la FAM, a Haiya alengezanso kuti bungweli lagulira ma galimoto atsopano omwe apeleka ku zigawo zake zitatu komanso ndi ku bungwe la Super League of Malawi (SULOM) ndi cholinga choti athandizire ntchito zawo pa masewelo.

Mtsogoleri wa FAM-yu wapempha adindo kuti agwiritse bwino ntchito ma galimoto amene apeleka kwa nthambizi ndipo ati posachedwapa akhale akulemba oyendetsa ndi okonza galimotozi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.