Banja langa layamba kusokonekera chifukwa cha matenda a TB – Gondwe

Advertisement
TB

A Anthony Gondwe omwe ali ndi zaka 52 ochokera kwa mfumu yaikulu Chikulamayembe m’boma la Rumphi ati banja lawo layamba kusokonekera pamene anawapeza ndi matenda a chifuwa chachikulu cha TB, chaka chatha.

Poyankhurana ndi a Gondwe, anati chiwapezereni ndi nthenda ya chifuwa chachikuluchi, zinthu zambiri m’moyo wawo zinasintha chifukwa chosowekera mphamvu zokwanira zoti angathe kugwira ntchito, nkupeza chakudya chapakhomo ngati umo amachitira kale adali walunga.

Iwo anawonjezera ponena kuti pachifukwa chimenecho, a mayi akunyuma kwawo anayamba kuyankhura motsakhala bwino nkutenga udindo wa mwamuna , pamene iwo nkum’mawanyadzitsa ngati munthu wa mayi koma iwo sadandaura podzindikira kuti padakali pano mankhwala omwe anawapatsa kuchipatala akugwira ntchito kwambiri m’thupi mwawo. 

“Ngakhale zili chomwechi, ineyo ndikuona kusintha posiyanasina ndi kale. Kale ndimatuluka thukuta la mbiri ndikagona moti pogona ponse pamanyowa komano pano zinachepa. Mphamvu dzayamba kubwera ndipo nthupimu, ndipo ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti ndiyambanso kugwira ntchito. Aboma amatipatsa thandizo lonse kuphatikiza ndalama yamayendedwe pobwera kuno kuchipatala,” adatero pofokoza.

Wachiwiri kwa mkulu othana ndi chifuwa cha chikulu cha TB pa Chipatala chaching’ono cha Bolero a Martin Mulenga anati ndi okondwa kuti anthu ambiri anayamba kuyezetsa matendawa ndipo amene anapezeka ndi nthendayi anayambapo kulandira mankhwala motsatira ndondomeko yomwe iwo ngati chipatala amapereka. 

A Mulenga ati chiyembekezo chawo ngati Chipatala cha Bolero nchakuti akufuna anthu asamakhale ndi mantha komanso chikaiko pamene akubwera kudzayezetsa ncholinga choti adziwe ngati ali ndi chifuwa chichikulu kapena ayi popeza zotero zithandiza kuti matendewa agonjetsedwe.

Boma linakhazikitsa kuti pofika 2030 nthenda ya chifuwa chachikulu cha TB idzakhale yatha. Nthendayi imapedzeka mwa abambo, amayi komanso ana ndipo ndiyochizika.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.