M’busa amangidwa kamba kogwirira mwana odwala khunyu

Advertisement
CUFF

Apolisi m’boma la Mulanje  amanga m’busa Steven Zambia wazaka 38 Lachitatu pa 26 June  kamba  kogwirira mwana wa zaka 15 yemwe ndi odwala nthenda ya khunyu.

Mneneri wa apolisi ku Mulanje, Innocent Moses wauza Malawi24 kuti m’busayu adanamiza makolo amwanayu kuti ali ndi kuthekera kochiza nthenda ya khunyu yomwe mwanayu wakhala akudwala.

Mneneri wa apolisiyu wati m’busayu wakhala akuchita zadama ndi mwanayu kuchokera mwezi wa February kufikira mwezi uno wa June pomwe zadziwika kuti tsopano mwanayu ali ndi pakati.

Moses wati mtsikanayu amadwala nthenda ya khunyu  ndipo m’busayu adapita kunyumba kwa mtsikanayu ndikuwapempha makolo ake kuti azimutenga ndikukamupemphelera ku phiri komanso kunyumba kwake.

Iye atazindikira kuti wapatsa mtsikanayo pathupi, anapita kwa makolo ake n’kukafunsira ukwati.

Izi zinakwiyitsa makolo amwanayu omwe anakamang’ala za nkhaniyi ku polisi, ndipo pambuyo pake apolisi anagwira m’busayo kamba koti wakhala akugonana ndi mwana.

Posachedwapa m’busayu akaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe pa mulandu ogwilira mwana.

M’busa Zambia amakhala m’mudzi mwa Mkweya kwa mfumu yaikulu Mabuka ndipo amachokera m’mudzi mwa a Makaula kwa mfumu yaikulu Mabuka ku Mulanje.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.