Aphunzitsi ena ku Thyolo sanalandilebe ndalama atayang’anira mayeso a JCE

Advertisement
MANEB Exams

Aphunzitsi okwana 59 m’boma la Thyolo adandaula kuti bungwe loyendetsa mayeso la MANEB silikuonetsa chidwi chowapatsa ndalama zawo za alawasi pa ntchito yoyang’anira mayeso a JCE, pomwe anzawo ena analandira mayesowa asanayambe kulembedwa.

M’modzi mwa aphunzitsiwa yemwe wasankha kuti tisamutchule dzina, watiuza kuti aphunzitsiwa amayenera kulandira ndalama za alawasizi mayeso a Junior Certificate of Education asanayambe kulembedwa pa 4 June chaka chino.

Mphunzitsiyu wati chodabwitsa nchakuti iye pamodzi ndi aphunzitsi ena okwana 58 ochokera m’bomali sanalandirebe ndalamayi mpaka pano ngakhale kuti akuluakulu a maphunziro m’bomali anawatsimikizira kuti ndalamazi alandira mayeso a JCE omwe amayang’anira asanathe.

Iye wati, “Titayipeleka nkhaniyi kwa akuluakulu, anatiyitanitsa kuti tikaone ngati sitinalakwitse ma nambala athu aku bank koma panalibe yemwe analakwitsa. Kenaka anapanga gulupu la WhatsApp pomwe poyamba amatidziwitsa zomwe zikuchitika.

“Pano tikafusa sakutiyankha kanthu. Tikudabwa chifukwa anzathu omwe amayang’anira mayeso m’sukulu zomwe zinayandikana ndi nsewu analandira ndalama zawo mayeso asanayambike pamene ife amene tinali m’sukulu zakutali ndipo timagonera komweko sitinalandilebe mpaka pano.”

M’modzi mwa akuluakulu a maphunziro m’bomali a Wallace Goffat, atitsimikizira kuti aphunzitsi 59 sanalandiledi ndalama zawo za alawasi koma anati sakudziwa chomwe chachedwetsa ndipo anatikankhira ku bungwe la MANEB.

Ofalitsa nkhani ku bungwe la MANEB Angella Kashitigu, sanafotokoze mwamvemvemve chomwe chapangitsa kuti aphunzitsiwa asalandire ndalama zawo za alawasi mpaka pano, koma watsimikiza kuti bungweli likuyesetsa kuti likoze vutoli.

Kashitigu wati, “ngati anapeleka mavuto awo kwa akuluakulu asadandaule athandizidwa. Thyolo ndi limodzi mwa maboma omwe tikumalipira anthu kudzera m’njira za makono, ndiye ngati sanalandire mwina nkutheka ma nambala awo aku bank anali olakwika.”

Kashitigu watiso sakudziwa tsiku lenileni lomwe aphunzitsiwa angalandire ndalamazi koma watsutsa mphekesera zomwe zimaveka kuti zatelemu aphunzitsiwa adzalandira ndalamazi mayeso a MSCE akadzatha pa 26 July 2024.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.