Kalindo wamangidwanso

Advertisement
Bon Kalindo

Dzulo apolisi amanga mtsogoleri wagulu lomenyelera ufulu wa anthu la Malawi First a Bon Kalindo pa Kamuzu Road m’boma la Salima.

Malipoti akusonyeza kuti a Kalindo awamanga pa mlandu okhudza kufalitsa uthenga osayenera pamasamba a mchezo omwe mchingerezi umatchedwa kuti Cyber related crime.

A Kalindo apita nawo ku likulu la nthambi ya polisi ku Area 30 mu mzinda wa Lilongwe.

Pakadali pano akuluakulu apolisi sadayankhulepo kanthu pazokhudza kumangidwa kwa a Kalindo.

Mbuyomu a Kalindo adamangidwaponso pa nkhani yokhudza kuyambitsa ziwawa.

Advertisement