Loans Board yati ikukonza vuto lakuvuta kwa tsamba lopangira ndondomeko yopemphera ngongole 

Advertisement
MUBAS

Bungwe lopereka ngongole kwa ophunzira msukulu zaukachenjede la Higher Education Students Loans and Grants Board (HESLGB), lati likukonza vuto lakuvuta kwa tsamba la intaneti lochitira ndondomeko yopemphera ngongole.

Izi ndi malingana ndi uthenga omwe bungweri lalemba kudzera pa tsamba lake la m’chezo la Fesibuku.

Bungweli lati lidzadziwitsa ophunzirawa vutoli likakonzedwa. 

Kotero bungweli lapepesa kwa onse okhudzidwa kamba kamavuto omwe adza kaamba kakuvuta kwa tsambali.

Apa ophunzira ena apemphanso bungweli kuti liwonjezere masiku ochitira ndondomekoyi.

Ophunzirawa anena izi kudzera m’gawo la ndemanga kutsamba lake la m’chezo.

Advertisement