Chakwera wasankha Annabel Mtalimanja kukhala wapampando wa MEC

Advertisement
Justice Annabel Mtalimanja

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, asankha oweluza milandu ku bwalo lalikulu a Annabel Mtalimanja kuti atsogolere bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC).

Malingana Ndi kalata imene bungwe la MEC latulutsa lero yomwe atsimikizira ndi mneneli wa bungweli a Sangwani Mwafulirwa, pogwiritsa ntchito mphamvu za lamulo la nambala 75 la malamulo a dziko lino komanso lamulo nambala 4 la bungwe la MEC, a Chakwera asankha wapamphandoyu limodzi ndi ma Commissioner awiri a Rev. Philip Kambulire ndi a Limbikani Kamlongela.

A Mtalimanja alowa m’malo mwa oweluza milandu a Chifundo Kachali kutsatila kutha kwa nthawi yawo yogwilira ntchito limodzi ndi a Antony Mukumbwa komanso a Olivia Liwewe omwe anali ma commissioner a bungweli.

A Kachali analowa kukhala wa pampando wa MEC m’malo mwa oweluza mayi Jane Ansah kuti ayendetse zisankho za chibwereza zomwe zinachitikanso 2020 kutsatira chigamulo cha bwalo la milandu kuti zisankho za m’chaka cha 2019 zinali ndi zosokonekera zambiri.

Advertisement