Ophunzira adandaula ndikuvuta kwa tsamba lopemphera ngongole la Loans Board 

Advertisement
Chanco students

Nkhawa yakula kwa ophunzira a msukulu zaukachenjede ochuluka omwe sadachitebe ndondomeko yopemphera ngongole ku bungwe la Higher Education Students Loans and Grants Board (HESLGB) pamene tsamba lochitira izi silikutsegula angakhale kuti bungweli lidati litseka pa 30 June mwezi uno.

Kafukufuku omwe Malawi24 yapeza akuonetsa kuti ophunzira ochuluka sadachitebe ndondomeko yotengera ngongoleyi, angakhale kuti bungweli lidalengeza kuti litseka kumapeto amwezi uno.

 M’modzi mwa ophunzira yemwe anayankhulana ndi Malawi24, Paul Sapala, anati wakhala akuyesayesa kuti achite izi koma sizikutheka kamba koti tsambali silikutsegula.

Ophunzira wina anati kusowa kwa ndalama yomwe amalipira kuti apeze nawo thandizoli ndi mwa ena mwamavuto omwe ophunzirawa achedwa kupempha ngongoleyi.

Vutoli lakhudzanso ophunzira omwe angowasankhira kumene kuti akachite maphunziro msukulu zaukachenjede zamdziko lino kutsatira bungwe la National Council for Higher Education (NCHE) litatulutsa zotsatira zake ndipo amayenera kupempha ngongoleyi mwezi uno.

Malawi24 inayesa kuti iyankhulane ndi akuluakulu akubungweli koma manambala awo sadali kupezeka.

Advertisement