Munandilangizadi aMalawi koma ine kusava – walira Tay Grin 

Advertisement
Mutale Mwanza Zambian socialite in Malawi

Pomwe Mutale Mwanza wanenetsa kuti sanakhalepo pa ubwenzi ndi Tay Grin yemwe akuti ndi khanda komaso samatha kukonda mkazi, “mfumu ya zinyawu-yi” yati ikunong’oneza bondo posavera malangizo omwe anthu ankayipatsa kuti isachite chibwezi ndi nkazi wa ku Zambia-yu.

Tay Grin yemwe dzina lake lenileni ndi Limbani Kalilani, walemba izi lero Lachiwiri pa tsamba lake la fesibuku potsatira kuponyerana mawu komwe kwabuka pakati pa iye ndi chiphadzuwa chaku Zambia-chi, Mutale.

Nkhaniyi ysyamba potsatira zimene anayankhura Mutale posachedwapa mu kanema wina momwe anati sanagwepo m’chikondi ndi Tay Grin ponena kuti woyimba wa ku Malawi-yu ndi khanda kwa iye.

Mukanemayi Mwanza anati, “ndimapanga zibwezi ndi anthu akuluakulu, sindinapange chibwezi ndi Tay Grin. Iyeyu ndi mwana, akuyenera kupanga chibwezi ndi atsikana aku koleji (college).”

Kupatula apo, Mwanza walemba kangapo konse pa tsamba lake la fesibuku zonyogodora Tay Grin. 

Mwa zina nyenyeziyi yati mamuna amayenera adzikonda nkazi wake zomwe akuti Tay Grin samapanga.

Mawuwa atokosola mkwiyo wa mwini dambwe-yu yemwe kudzera pa tsamba lake la fesibuku wadziguguda pa chifuwa, kudandaula kuti sanavere malangizo omwe a Malawi ena ankamupatsa okhudza akazi a ku Zambia.

Woyimbayu walemba kuti; “Malawians tried to warn me (a Malawi anayesetsa kundilangiza), koma kusamva nane. I’m done with Zambian women (ndathana nawo akazi aku Zambia)”.

Pakadali pano, kusinthana mawu kwa Mutale ndi Tay Grin kwayambukira kwa anthu a m’dziko la Zambia komaso Malawi omwe aliyese akumayikira kumbuyo munthu wa m’dziko la kwawo zomwe zapangitsa tsamba la fesibuku m’mayiko awiriwa kutekeseka.

Tay Grin ndi Mwanza akhala ali paubwezi kuyambira mu October chaka chatha. Anthu anadziwa za ubwezi wa awiriwa kamba ka zithuzi zachikondi zomwe awiriwa amaziponya m’masamba awo anchezo.

Advertisement