Mwambo wa maliro a Hope Chisanu uchitika mwezi uno ku America

Advertisement
Hope Chisanu

Pomwe anthu akupitilirabe kusonkha ndalama zokwana 43 miliyoni kuti thupi la malemu Hope Chisanu lifike kuno, anthu m’dziko la America atsazikana ndi malemuyu kumapeto a mwezi uno.

Chisanu yemwe wasiya mkazi ndi ana awiri, anamwalira Loweluka pa 1 June 2024 atadwala kwa nthawi yochepa m’dziko la America komwe amakhala.

Potsatira imfayi, akubanja anakhazikitsa ntchito yosonkhetsa ndalama zokwana $25,000 zomwe ndi zopitilira K43 miliyoni kuti thupi la malemuwa lifike kuno ku mudzi.

Patsamba la gofundme pomwe ndalamayi imasonkhedwa, kufikira lero papezeka ndalama zokwana $3,932 zokha basi zomwe ndi pafupifupi K7 miliyoni mwa K43 miliyoni yomwe ikufunika kuthupili lifike kuno ku mudzi.

Pakadali pano omwe akuyendetsa mwambo wa malirowa alengeza kuti mwambo wa maliro a Chisanu uchitika Loweluka pa 29 June 2024 m’dziko la America komwe anamwalilira.

Dongosolo la maliroli likusonyeza kuti mwambo otsazikana ndi a Chisanu ku America uchitikira m’dera lotchedwa 300 S 3RD ST RENTON, WA 98057 m’dzikolo.

Pakadali pano tsiku lomwe thupi la a Chisanu libwere kuno ku mudzi silinadziwike.

Chisanu anagwira ntchito ya uwulutsi ku wayilesi ya boma ya MBC ndipo kamba ka mawu ake opatsa chikoka komaso okhathamira, ankadziwika kwambiri ndi dzina loti “Uncle Bemberezi.”

Kupatula apo, malemuwa anali namatetule pa nkhani ya zisudzo ndipo anatenga nawo magawo akuluakulu m’ma kanema a ‘The Last Fishing Boat’ komaso yomwe yatulutsidwa posachedwapa ya ‘Is The President Dead?’.

Advertisement