Ndizopweteka kuti a Chilima salankhura pa mwambo uno monga momwe mayi Dzimbiri ankafunila – Njawala

Advertisement
Patricia Shanil Dzimbiri funeral

Ofalitsa nkhani za chipani cha UTM a Felix Njawala ati malemu Patricia Shanil Dzimbiri asanamwalire adalemba mbiri yomwe iwo ankafuna kuti anthu omwe adzafike pa maliro awo adzatsatire.

Iwo ati ndizokhudza kwambiri kuti mwa zina zomwe iwo amkafuna ndi zoti omwe adzayankhule pa Maliro awo adzakhale a Dr. saulos Klaus Chilima.

Koma akuti izi ndi zokhudza kwambiri chifukwa tsiku la lero a Chilima kulibe.

A Njawala akuti akuyankhula pa mwambowu poimilira Dr.Chilima ndipo ati zomwe iwo akuyankhula ndi zomwe akungoganiza chabe kuti a Chilima adakayankhula.

Mwazina, a Njawala ati malemu Dzimbiri anali munthu odzichepetsa kwambiri.

A Njawala alankhulaso kuti a Dzimbiri anali munthu okonda mtendere komanso kupemphera.

Advertisement