A Zikhale Ng’oma  komanso a Harry Mkandawire asatsogolere nawo mwambo wa maliro- atero aphungu a UTM

Advertisement
Ken Zikhale Ng'oma

A phungu komanso makhansala ochokera ku chipani cha United Transformation Movement (UTM) ati nduna ya chitetezo a Harry Mkandawire komanso a Ken Zikhale Ng’oma asakhale nawo otsogolera mwambo wa maliro a wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima omwe anamwalira Lolemba pa ngozi ya ndege.

Poyankhura pa msonkhano wa a tolankhani lero ku Lilongwe, aphunguwa omwe achokera ku Blantyre, Lilongwe, Mzuzu komanso maboma ena ati nduna ziwirizi zaonetsa kuti ndizosakhulupirika chifukwa sanatengepo gawo lalikulu pamene anamva nkhani yangoyizi.

Iwo awonjezera ponena kuti a Zikhale N’goma komanso a Mkandawire amayenera kukhala patsogolo pa zinthu zonse wina aliyense asanayambe kupereka mauthenga a ngoziyi chifukwa ndi  ntchito imodzi ya unduna wawo.

“Ngozi inachitika cha m’ma 10 koloko m’mawa kamano uthenga ochokera kwa a purezidenti a Lazarus Chakwera unalengezedwa usiku 11 koloko kusonyeza kuti mauthenga amabwera mochedwa kwambiri,” anatero pofotokoza.

Iwo ati anthu otsatira chipanichi komanso a Malawi onse ali ndi mafunso ochuluka komanso opanda mayankho potengera kuti zinthu zambiri zikuyenera kufufuzidwa.

Aphunguwa apempha anthu onse omwe amatsatira chipani cha UTM kuti asunge bata kulikonse komwe ali pa nyengo yazovutayi.

A Chilima komanso anthu ena asanu ndi atatu amwalira pa ngozi ya ndege lolemba mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Advertisement