Mayi wasiya mwana obadwa kumene pa chipatala cha Salima

Advertisement
Malawi24.com

Mayi wina  wasiya mwana wongobadwa kumene pa chipata cholowera pa chipatala chachikulu cha boma la Salima mbandakucha wa lero.

Mneneri wa a polisi m’boma la Salima a Rabecca Ndiwate wati apolisi Apolisi ku Salima akufunafuna mayiyu.

A Ndiwate ati mlonda yemwe amgwira ntchito ya usiku pachipatapo anamva mwana akulira chapafupi ndi pomwe iye anali ndipo analondola kuti akaone.

Nkhaniyi inawapeza apolisi nawo anathamangira kumalowa kukaona.

Mwanayu akulandira chisamaliro choyenera kuchipinda chomwe amasungilako ana pachipatalachi ndipo apolisi akusakasak mayi ake amwana.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.