Musatiipitsile mbiri, ife anthu aku Ntcheu sitinakutumeni – munthu wina wauza Norman Chisale

Advertisement
Norman Chisale former presidential bodyguard

Nzika ina ya m’boma la Ntcheu yadzudzula mkulu wa chitetezo wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Peter Mutharika, a Norman Chisale, powuza dziko kuti anthu m’bomali diokwiya pakuzuzidwa kwa nzika zake zina.

Izi zikudza pomwe posachedwapa a Norman Chisale omwe amachokera m’boma la Ntcheu, anauza wayilesi ya Zodiak kuti anthu m’bbomali ndiokwiya kwambiri kamba ka zomwe anthu andale akuchitira nzika zina zotchuka za m’boma lawo.

A Chisale anapeleka chitsanzo cha kumangidwa kwa iwo, kumangidwa kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima komaso kusatha kwa milandu ya mneneri Shepherd Bushiri, ngati zina zomwe zakwiyitsa angoni a m’boma la Ntcheu ndipo anati anthu onsewa kuphatikiza iwo akuzunzika pa zifukwa za ndale.

Apa mkuluyu anati ndizachidziwikire kuti anthu m’bomali sangakhale osangalala kumaona azibale awo monga ngati iwo, a Chilima komanso a Bushiri akuzunzidwa ndi boma pazifukwa za ndale ndipo anatsindika kuti anthu m’bomali ndiokwiya zedi.

Koma nzika ina yotchuka m’bomali a Wester Kosamu adzudzula a Chisale kamba ka zomwe anayankhulazi zomweso ati ndi bodza la nkhunkhuniza komanso ati ndizotsutsana ndi chikhalidwe cha angoni a m’bomali.

A Kosamu omwe anayankhula izi kudzera pa tsamba lawo la fesibuku, anati ndiodabwa kuti a Chisale akupakiliza nzika za m’boma la Ntcheu pa mkwiyo omwe iwo ali nawo pa boma lotsogozedwa ndi a Lazarus Chakwera ndipo apitilira ndi kunena kuti uku ndikuwalakwira angoniwa omwe wati amakhulupilira umodzi.

Apa mkuluyu anauza a Chisale kuti asayipitsile mbiri anthu m’bomali ndipo wati anthu m’bomali sanatume mkuluyu kuti awayankhulire.

“Anthu aku Ntcheu sitinatume munthu kuti adziyankhula mmalo mwa ife ndipo mbava kulibeko. Mbambadi kwathuku mukapeza ma Judge, ma loya, madokotala, aphunzitsi, ma board Chair, ma CEO, ma Impi, ma Makosi aulemu wawo ndi Madolo ambiri olemera mwachilungamo  komanso kuphunzira bwino. Musatiwonongere mbiri angonife cheketedi pangani zanu,” Kosamu wuza a Chisale

Munthu wina yemwe anaikira ndemanga pa zomwe a Kosamu analemba pa tsamba lawo la fesibuku, anati ndiodabwa kwambiri kuti a Chisale amanamiza anthu m’dziko muno bukhu lopatulika lili m’manja mwawo.

Pomwe wina anati: “Mbambadi angoni, hez just seeking sympathy from us (akungofuna tiwamvere chisoni), akuntcheufe,angonife”

Advertisement