Apolisi akusakasaka dalaivala yemwe analanda mfuti ya wapolisi

Advertisement
Firearm belonging to Malawi Police

Apolisi mu mzinda wa Lilongwe akusaka dalaivala wa truck, Grey Chisinga, yemwe akuti analanda mfuti ya wapolisi wina pa nthawi imene apolisi anamanga dalaivalayu pa mlandu ozembetsa feteleza.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ku Central West Region Police, a Foster Benjamin, ati a Chisinga akuganiziridwa kuti anagulitsa feteleza opyola matumba 600 yemwe adanyamula kuchoka ku Blantyre kupita ku Kanengo.

Dalaivalayu adayisiya truck yopanda kanthu pa Six Miles ku Lilongwe iye ndi kuthawa.

Apolisi adasaka a Chisinga ndipo atawagwira anawatengera komwe kunali truck yawo ndipo anawauza ayendetse apite limodzi ku polisi.

A Chisinga omwe anagwirapo ntchito yapolisi anayamba kuyendetsa koma atafika pa mlatho wa pa mtsinje wa Lilongwe omwe uli ku msewu wa Bypass, iwo anaimitsa galimotoli ponamizira kuti laonongeka.

Anthuwa anatsika ndikuyamba kugwiragwira galimotoyo koma apa Chisinga anapeza mwayi olanda mfuti yawapolisiyo.

Iwo anaombera kawiri koma mwamwayi anamuphonya wapolisiyo ndipo iye anapeza mpata othawa ndikubisala.

Kenaka a Chisinga anaimitsa wa njinga ndikumukakamiza kuti awathawitse molowera ku dera la 36 ku Lilongwe.

Naye wapolisiyu anadumphira pa njinga nkuyamba kuthamangitsana ndi a Chisinga.

Koma a Chisinga amaomberabe ndipo wanjinga yemwe anawanyamula anawatsitsa poopa kuti zipolopolo zingamuvulaze.

Chisinga atatsika njingayo anathawa ndipo sakudziwika komwe analowera.

Padakadali pano apolisi apeza mfuti yomwe a Chisinga analanda koma ili ndi zipolopolo zitatu zokha mwa zipolopolo khumi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.