CDC Investment yabanduka ndi ndalama za gulu

Advertisement
CDC scam Malaw

Anthu omwe amasunga ndalama pa kampani ya pa intaneti ndicholinga chofuna kupeza phindu phwamwamwa, manja ali ku nkhongo kwinaku akudziguguda pa mtima kuti ndinkaganiza chiyani ine pomwe zikumveka kuti kampani ya CDC Inves yabowola mtambo ndi ndalama za gulu za nkhani-nkhani.

Mphekesera zikusonyeza kuti kampani ya Cryptopro yomwe imatchukaso ndi dzina loti CDC Investment yawulutsa ndalama zomwe anthu amapanga invesiti (invest) kudzera pa intaneti.

Malipoti akusonyeza kuti tsamba la pa intaneti ya kampaniyi komwe anthu amayika ndalama zawo ndikumadikira kuti zichulukane ngati nchenga, yasiya kugwira ntchito zomwe zikupeleka chiwopsezo kuti a Malawi ambiri apangidwa utsizinamtole.

Pakadali pano tsamba la kampaniyi silikupezeka pa intaneti zomwe zapangitsa kuti anthu omwe anasunga ndalama zawo asakwanitse kowona kapena kutenga ndalama zomwe anapanga invesiti-zo.

Izi zikudza pomwe ena amadalira kuti posachedwapa moyo usintha kamba ka phindu lochokera ku kupanga invesiti ndalama zawo ku kampani ya CDC Coin.

Ngakhale zili choncho, anthu ena pa masamba anchezo a kuti bungweli silinathawitse ndalama za anthuzi koma kuti lakumana ndi vuto lomwe a kuti akulikoza.

Malipoti ena osatsimikizikaso akusonyeza kuti tsamba la kampani ya Cryptopro lidzayambaso kugwira ntchito pa 23 November, 2023.

Advertisement