Tikumangani mukamafalitsa kuti Kunkuyu akukhuzidwa ndi imfa ya Witika – atelo apolisi

Advertisement

Apolisi m’dziko muno ati amanga aliyese amene apitilire kufalitsa nkhani zonama kuphatikiza yoti nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa Allan Witika mwezi watha.

Izi zili muchikalata chomwe nthambi ya yosungitsa chitetezoyi ya Malawi Police Service (MPS) yatulutsa lolemba pa 23 October, 2023 chomwe wasainira ndi ofalitsa nkhani wa nthambiyi a Peter Kalaya.

M’masamba anchezo ochuluka mwakhala mukuzungulira kilipi ina yomwe oyankhulayo akuti a Kunkuyu akukhudzidwa ndi kuphedwa kwa Witika yemwe anali ogwira ntchito ku kampani ya Coco-Cola Beverages.

Mphekeserazi zili mkati, nawo apolisi posachedwapa amanga a Lester Maganga, mthandizi wa a Kunkuyu, powaganizira kuti anatenga nawo gawo pa kuphedwa kwa Witika.

Koma apolisi ati kufika pano sanalandire umboni uliwonse omwe ukuwonetsa kuti ndunayi ikukhudzidwa ndi kuphedwa kwa Witika monga momwe zakambidwira mu kilipi yomwe pano anthu akuyigawana kwambiri.

Munchikalatachi a Kalaya achenjeza anthu m’dziko muno kuti asiyiletu nchitidwe ofalitsa nkhani zopanda umboni, ndipo ati aliyese amene apezeke akupanga choncho, anjatidwa ndikuzingedwa mlandu.

“Nthambiyi ili ndi nkhawa yaikulu kuti anthu ena akufalitsa dala uthenga wosocheretsa omwe akutchulamo anthu osalakwa womwe ndi mlandu wolangidwa ndi lamulo.

“MPS ilibe umboni uliwonse wokhudzana ndi a Hon Moses Kunkuyu, nduna yofalitsa nkhani pamilandu yomwe ikufufuza monga momwe wina akunenera pa kilipi yapa WhatsApp yomwe ndi yosocheretsa. Nthambiyi pakadali pano ikutsatira omwe apanga kilipi yosocheletsayi. Akamangidwa, adzaimbidwa mlandu malinga ndi lamulo la Electronic Transactions and Cyber-Security Act,” yatelo kalata ya apolisiyi.

Padakalipano, bwalo la majisitileti lalamula kuti mlandu wa a Maganga upite ku bwalo lalikulu kaamba koti mlanduwu ndi waukulu. Bwalolo lati a Maganga akhale pa alimandi ku ndende ya Maula kwa masiku 90 kuti apolisi amalize kufufuza kwawo.

Advertisement