Bambo owotcha makala wafa ndi mpweya oyipa

Advertisement

Ku Mangochi bambo wa zaka 32 wamwalira atapuma mpweya oyipa ochokera mu utsi pamene amaotcha makala m’nkhalango ina.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi omwe azindikira mzobamboyu ngati a Salabadika Kauma.

A Tepani Daudi ati ngoziyi yachitika lamulungu pa 22 October 2023, m’nkhalango ya Namizimu yomwe ili m’dera la mfumu yayikulu Katuli m’bomali.

Msuweni wa malemuwa anauza apolisi kuti bambo Kauma, yemwe anali katakwe pa nkhani yowotcha makala m’derali, adapita kunkhalangoyi yekha pa 18 October, 2023 kuti akapange monga mwa nthawi zonse.

Koma chodabwitsa nchakuti nkuluyu sadabwerenso ku nyumba kwake ndipo patadutsa masiku awiri, akubanja adadziwitsa a polisi ya Katuli za kusowa kwa m’balewawoyu.

Apa a polisiwa sadachedwe ndipo mothandizana ndi anthu am’mudzimo, anakhazikitsa ntchito yofufuza komwe bambo Kauma anali.

A Tepani Daudi ati mtembo wa bambo Kauma unapezeka lamulungu koma anupeza pa mtunda wamakilomita 20 kuchokera pomwe amaotchela makala mu nkhalango ya Namizimu.

A polis ati zotsatira za chipatala cha Katuli zawonetsa kuti bambo Kauma adakomoka chifukwa chopuma mpweya wa carbon monoxide womwe udapuma panthawi yomwe amaotcha makala.

Bambo Salabadika Kauma anali ochokera mmudzi mwa Nsalure, mdera la mfumu yaikulu Katuli m’boma la Mangochi.

Advertisement