Bambo wafela ku lumu atamwa mankhwala opereka mphamvu kwa bambo

Advertisement
Malawi24.com

Apolisi m’boma la Mulanje atsimikiza kuti bambo wina wa zaka pafupifupi 70 wamwalira mkati mwa ndime ku malo ena ogonako alendo pomwe anamwa mankhwala opeleka mphamvu kwa abambo.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mulanje a Innocent Moses omwe azindikira zibamboyu ngati a Leman Walama.

Moses wati bambo Walama apezeka atafa m’mawa wa lachitatu pa malo ena ogonera alendo omwe ali pa malo ochitila malonda a Chitakale mbomali.

Apolisi ati bamboyu anamwa mankhwala opeleka mphamvu kwa abambo kenaka ndikupita ku maloko ndi mayi wina.

Malingana ndi a Moses omwe anayankhula ndi nyumba zina zofalitsira nkhani mdziko muno, bambo Walama amwalira alinkati mochita za dama ndi mayiyo.

“Bamboyu wamwalira nkati mwa masewerowo, ndipo titalandira lipotilo, tidathamangira komweko ndikukatengera mtembowo ku chipatala cha m’boma la Mulanje, komwe zotsatira zawonetsa kuti imfayi idachitika chifukwa cha matenda a mtima,” atero Moses poyankhula ndi nyumba ina yofalitsa nkhani.

Pakadali pano, thupi la malemuyu likadali ku chipatala cha Mulanje kudikila achibale kuti adzetenge thupili.

Apolisi ati malemu Walama amachokera m’mudzi mwa Gulumba, mfumu yayikulu Chikumbu m’boma la Mulanje.

Advertisement