Bambo wa zaka 40 amugamula kukhala ku ndede zaka 12 pa mulandu wogwilirira

Advertisement

Bwalo la milandu ku Chiradzulu lagamula a Matias Kabango a zaka 40 kukakhala kundende kwa zaka 12 chifukwa chogwilira mwana wa dzaka 16.

Mneneri wa a polisi ku Chiradzulu a Cosmas Kagulo anati oimila boma pa mulanduwu a Spenard Chankoma anauza bwaloli kuti pa 12 Ogasiti chaka chino a Kabango anamugwilira mwanayu pamene anali kumunda kosaka nkhuni.

Koma a Kabango anaukana mulanduwu zomwe zinapangisa oimila boma kuitana mboni kuzatsimikizila zachiwembuchi.

Popeleka chigamulo, oweruza milandu a Smart Maruwasa anawapeza a Kabango kuti ndi olakwa ndipo kuti akakhale kundende kwa zaka 12.

A Kabango amachokela mudzi wa a Njeremba, Mfumu yaikulu Likoswe boma lomwelo la Chiradzulu.

Advertisement