Adindo adandaula ndikusowa kwa zipangizo zochotsela zinyalala pa msika wa Namadzi

Advertisement
People in Chiradzulu have cleaned up Namadzi Market in the district

Adindo ena pa msika wa Namadzi ku Chiradzulu adandaula ndikusowa kwa zipangizo zochotsela zinyalala monga mawilibala ndi mafosholo pamsikawu.

A George Mkwate m’modzi, wa mamembala a komiti pamsikawu wati mawilibala, mafosholo komanso zotchinga kukamwa ndi zina mwa zinthu zomwe alibiletu pamsikawu.

“Kusowa kwa zinthu zimenezi kumaika moyo wathu pa chiopsezo cha matenda osiyanasiyana,” adatero a Mkwate.

Poyankhapo, mkulu wa Chiradzulu Development Group a Louis Banda wati madandaulowa amveka ndipo kuti adziwitsa anthu oyenelera kuti mavutowo athe.

Iwo analimbikitsatso anthu pamsikawu kuti azitengapo gawo posamalira malo osiyanasiyana ku madela omwe amachokela.

Boma la Malawi m’mbuyomo lidakhadzikitsa mchitidwe osamalira ndikusesa m’mizinda komanso malo ena sabata yachiwiri ya mwezi wina uliwonse.

Advertisement