Nkokenkoke ku bwalo la milandu ku Chiradzulu

Advertisement
Malawians at a court in Chiradzulu

Kunali mkokekoke ndi maphokoso ochuluka kuchokera  kwa otsatila oganizilidwa milandu pamene oweruza milandu ku Chiradzulu anakana kupereka belo kwa anthu 15 omwe akuzengedwa milandu yakuba ndi kuononga katundu wa esiteti ya Mulli.

Anthuwa adandaula kuti oweruza milanduyi yemwe dzina lake ndi Smart Maluwasa wakana kupeleka belo ngakhale kuti mboni zaboma zopitilira zitatu zati zikuzindikilapo anthu awiri okha pa anthu 15 omwe akuzengedwa milanduyi.

Sabata latha pa 2 Okotobala anthu ena a m’mudzi mwa Mfumu yaikulu Chitera anaononga Esiteti ya Mulli ndi kuba ndalama zokwana 500 sauzande kwacha.

Oweruza milandu ku bwaloli azapitilira kuva mulanduwu pa 19 mwezi omwe .

Wolemba Andrew Salima – Chiradzulu

Advertisement