Njobvu yavulaza munthu ku Kasungu

Advertisement
Elephants Malawi

Mfumu Kapelura ya m’boma la Kasungu yati imodzi mwa njobvu zomwe zinatuluka mu nkhalango ya Nkhotakota yavulaza munthu mdera lawo.

Malingana ndi mfumuyi, njobvu zisanu ndi ziwiri ndi zomwe zinatuluka ku nkhalango yotetezekayi ndi kulowa m’mudzi mwawo lachinayi.

Iwo anati anthu anachita chidwi ndi njobvuzi ndipo anayamba kuzilondola pamene ena amazigenda ktui zibwelere ku nkhalango.

”Anthu ali mkati mozilondora, Njovu ina inagunda munthu ndipo mwamwayi wake anagwera mu dzenje lomwe linali pafupi zomwe zinapangitsa kuti isamuone pomwe imafuna imuponde,” inatero mfumuyi polankhulana ndi wayilesi ya Kasungu komunite.

Iyo inawonjezera kunena kuti ovulazidwayu amugoneka pa chipatala chachikulu cha boma la Kasungu

Njobvuzi akuti zaononganso dimba lomwe zinalowamo.

Padakali pano, mkulu wa nkhalango ku Nkhotakota David Nangoma wauza kanema wa Mibawa kuti njobvuzo zabwelera ku nkhalango ya nkhotakota. A Nangoma achenjeza kuti apewe kulondola njobvu komanso kuziopseza.

Advertisement