Ophunzira pa Ntcheu Sekondale atopa ndi chakudya chowawa

Advertisement
Ntcheu secondary school

Pena munthu umafikadi potopa ngati momwe atopera ophunzira pa sukulu ya boma ya Ntcheu sekondale omwe adandaula kuti chitsekulireni sukuluyi mwezi watha, akupatsidwa chakudya chowawa kwambiri.

Izi zadziwika lero la chiwiri pa 10 October pomwe ophunzirawa anatengana onse ndikupita ku ofesi ya mkulu wa za maphunziro m’bomali kukatula madandaulo awo okhudza chakudya chomwe akupatsidwa.

Ena mwa ophunzirawa ati chitsekulireni sukuluyi pa 11 September mwezi watha, akudya phala komanso nsima zowawa kwambiri.

Ophunzirawa ati ngakhale akhala akuwuza akuluakulu pa sukuluyi za vutoli, palibe chomwe chikuchitika ndipo ati ndi chifukwa chaka opanga chiganizo chothamangira ku ofesi ya mkulu wa maphunziro m’bomali.

Iwo ati akukhulupilira kuti mkulu wa maphunziro m’bomali ali ndikuthekera kopangitsa kuti zomwe akhala akudandaulazi zisinthe.

Kanema wina yemwe anthu akugawana m’masamba anchezo akuwonetsa ophunzirawa atatengana ndi kutuluka msukuluyi ndikumathamangira ku ofesi ya mkulu wa maphunziro m’bomali kukatula nkhawa zawo.

Izi zikubwera patadutsa masiku ochepa pomwe ophunzira oposa makumi anayi anatengedwera ku chipatala pa sukulu ya Lunzu munzinda wa Blantyre pomwe amaganizira kuti anadya chakudya chomwe munali poyizoni.

Advertisement