
Ngati a Peter Mutharika amayesa kuti akadutsa moyela ku convention yawo, apa ndiye aganize kawiri. A Kondwani Nankhumwa sali mocheza ndipo ati akawaswa a Mutharika.
Malinga ndi wailesi ya Zodiak, a Nankhumwa ati iwo sabwelera pambuyo ndi lingaliro lawo lofuna kutenga chipani cha DPP ndinso dziko lino mu 2025.
A Nankhumwa amene ndi mtsogoleri wa aphungu otsutsa ku nyumba ya malamulo analengeza kuti ali ndi khumbo lotenga utsogoleri wa DPP. Iwo adanena izi pamene zidamveka kuti a Mutharika akuganiza zopuma pa ndale.
Koma lamulungu lomweli, a Mutharika adaonetsa kuti iwo ayimilanso. Pa mwambo wa Mulhakho wa aLomwe a Mutharika ananena kuti 2025 akabwelera mu boma zinthu ziyenda bwino.
Atafunsidwa a Nankhumwa ngati ayimire kupikisana ndi a Mutharika, iwo ati atsimikiza kuti atero.
“Achita bwino ndipo kuyimira kuti ndiwathibule bwino. Ine sindimaluza masankho ndipo,” anatero a Nankhumwa.
Anthu ena amene akuonetsa chidwi mu utsogoleri wa DPP monga a Dalitso Kabambe ndi a Bright Msaka adanena kuti ngati a Mutharika akuyima, iwo sapikisana nawo. Koma a Nankhumwa ati sakubwelera m’mbuyo.
A Nankhumwa adanenaponso kuti iwo sikuti angotenga chipani cha DPP ayi, komanso utsogoleri wa dziko lino mu 2025.