Mafuta ngambwingambwi akubwera lolemba lomweli – atero a boma

Advertisement
Malawi hit with fuel crisis

Mizere yonse mukuyionayi, ati mukuyiona komaliza. Kuyambira lolemba lomweli ili, mafuta akhala paliponse moti malo omwetsera mafuta azichita kuyitanira anthu. Atelo ndi a boma.

Malinga ndi mlangizi wa a Chakwera a Ephraim Chibvunde, mafuta osowa pokhala akubwera mu dziko muno ndipo zogona pomwetsera mafuta zitha.

A Chibvunde auza nyumba youlutsa mauthenga ya Times kuti anthu ku boma akupanga chilichonse chotheka kuti mafuta afike mu dziko muno. Iwo ati ngakhale a Chakwera sakugona tulo Kamba ka vuto la kusowa kwa mafuta limene likubwerabwera mu dziko muno.

Vehicles on a queue at a fuel service station in Malawi. The country has been facing recurring fuel shortages for close to two years
Mizere yonse mukuyionayi, ati mukuyiona komaliza – Atero atsogoleri a Boma

Koma mosiyana ndi zimene a banki yaikulu ya dziko lino anakamba zoti mafuta akusowa Kamba koti dziko lino liribe ndalama zakunja, a Chibvunde ati pali anthu amene akuchita chipongwe boma la a Chakwera kuti lioneka lolephera. Anthu amenewa ati ndiamene akusowetsa mafuta mu dziko muno.

Iwo aopseza kuti boma liwapeza anthu amenewa ndipo liwaonetsa chimene chinameta nkhanga mpala.

Kuyambira kumayambiliro kwa sabata lino, mafuta a galimoto maka a Petulo akhala akusowa. Zinayambira ku Blantyre koma tsopano zikuoneka kuti sizinasiye malo ndipo dziko lonse likulilira mafuta.

Advertisement