Wagwa mpesa; chinkulirano chabuka ku SDA yakum’mwera

Advertisement

Maranatha! chikondi cha pa abale chipitililebe: mpungwepungwe wabuka mumpingo wa Seventh Day Adventist pomwe akuluakulu a mchigawo chakumwera alavula nthambi ya Bangwe kuti simbaliso imodzi ya mpingowu ponena kuti ikuchita kusaweruzika.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe akuluakulu a mpingo wa SDA mchigawo chakummwera atulutsa pa 22 September, 2023 chomwe wasayinira ndi mtsogoleri wa mpingowu mchigawochi a Wyson Thomas.

Mukalatayi, a Thomas ati akuluakulu a mpingowu mchigawochi anakumanapa 17 September chaka chino komwe anakakambirana za nkhani yoti Bangwe SDA ikuchita kusaweluzika.

Malingana ndi chikalatachi, mpingo wa Bangwe SDA, ukudzudzulidwa kamba kobweretsa ziphuzitso zachilendo zomwe a kuti ndizotsutsana ndi zikhulupiliro za mpingowu muno m’Malawi.

A Thomas ati potsatira nkumano okhudza nkhaniyi, akuluakulu a SDA mchigawo cha kummwera apanga chiganizo choti achotse nthambi ya Bangwe SDA mu nkaundula wompingowu mchigawochi.

R4rrr, dd
“Kutsatira Komiti Yaikulu ya South Malawi Conference yomwe inakumana pa 17 September, 2023, ndikulembera ndikudziwitsa matchalitchi onse a Seventh-day Adventist mdera lathu ganizo lomwe latengedwa loletsa kuchita chili chonse ndi Bangwe SDA Church kuyambira pano.

“Lingaliro lakanthawili lafika chifukwa cha kulimbikitsa kwake mosalekeza ziphunzitso zotsutsana ndi zikhulupiriro za mpingo wa Seventh-day Adventist,” yatelo mbali ina ya chikalatacho.

Kalatayi ikuletsa anthu ampingowu kuchokera ku nthambi zina mchigawachi kupita ku Bangwe SDA kukakhala nawo pa mapemphero kapena zochitika zili zonse za mpingo.

“Mwakulumikizana uku, mipingo yonse ya Seventh-day Adventist, magulu ampingo, kapena mamembala omwe ali okhazikika akulangizidwa kuti asapite ku tchalitchi cha Bangwe SDA kuzochitika zina za tchalitchi.

“Momwemonso, pempho lililonse lochokera kwa a Bangwe lofuna mautumiki aliwonse ochokera kumpingo, magulu ampingo kapena munthu paokha, SIZIYENERA kuvomerezedwa,” yateloso mbali ina ya kalatayi.

Akuluakulu a mpingowu mchigawochi ati ziletso zomwe aperekazi zikhalapo mpaka pomwe ofesiyi ikhaleso pansi ndikupanga chiganizo chokhazikika cha tsogolo la mpingo wa Bangwe SDA posachedwapa.

Advertisement